Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
  • Results
  • Related
  • Featured
No results found for: "".
  • Weighted Relevancy
  • Content Sequence
  • Relevancy
  • Earliest First
  • Latest First
    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents

    MUTU 4—KUBVOMEREZA

    “WOBISA macimo ace sadzaona mwai; koma wakuwabvomereza, nawasiya adzacitidwa cifundo.” (Miyambo 28: 13. ) Makhalidwe a kulandirira cifundo kwa Mulungu ali ofewa ndi olungama ndi oyenera. Yehova satifunsa ife kucita cinthu cacikuru kuti tilandire cikhululukiro ca macimo. Sitifunika kutoyenda maulendo atari ndi otopetsa, kapena, kucita zina zopweteka, kupereka miyoyo yathu kwa Mulungu wa kumwamba, kapena kupembedzera zoipa zathu; koma wakuwabvomereza ndi kuwasiya macimo ace adzacitidwa cifundo.MOK 27.1

    Mtumwi ati, “Cifukwa cace mubvomerezane wina ndi mnzace macimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzace kuti muciritsidwe.” (Yakobo 5: 16. ) Bvomerezani zoipa zanu kwa Mulungu, amene angathe kukhululukira, ndi zolakwa zanu kwa wina ndi mnzace. Ngati walakwira mnzako, kabvomereze kwa mnzako yemweyo ndipo ndi nchito yace kukukhululukira iwe. Pompo ukafunse cikhululukiro kwa Mulungu, cifukwa mnzako wamcimwirayo ndi cuma ca Mulungu, ndipo pakumpweteka iye wacimwira Mlengi wace ndi Mombolo wace. Mlanduwo umatengedwa pamaso pa Mnkhoswe woona, Mkuru Wansembe wathu, amene “anayesedwa m’zonse monga momwe ife koma wopanda ucimo, ndi amene “amamva cifundo ndi zofooka zathu” (Heb. 4: 15), ndipo ali wakutha kutsuka cimo liri lonse.MOK 27.2

    Iwo amene sanapereke miyoyo yawo pamaso pa Mulungu pa kubvomereza zoipa zawo, sanaponde khwelero loyamba la kulandiridwa. Ngati ife sitinalape cotero, ndipo sitinabvomereze zoipa zathu ndi mzimu wosweka ndi wodzicepetsa, ndi kunyansidwa nazo mphulupulu zathu, sitinacifune moonadi cikhululukiro ca macimo; ndipo ngati sitinacifune, sitinaupeze mtendere wa Mulungu. Cifukwa cace cimene sitimasuka ku zoipa zathu za kale, ndi cifukwa cakuti sitiri olola kucepetsa mitima yathu ndi kuyanjana ndi macitidwe a mau a coonadi. Malangizo anafotokozedwa mokwana za mlandu umenewu. Kubvomereza macimo ngakhale pa anthu ambiri kapena mtseri, kudzikhala kocokera mu mtima, ndi kofotokozedwa bwino lomwe. Wocimwayo asamakakamidzidwa. Asamangonena mosasamala, kapena kukakamizidwa ndi iwo amene sazindikira kunyansa kwace kwa ucimo. Kubvomereza kumene kumacokera pansi pa mtima kumapeza njira yopita kwa Mulungu wa cifundo cosatha. Davide ati, “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34: 18. )MOK 27.3

    Kubvomereza koona masiku onse nkwa makhalidwe odziwika bwino kochula zoipa zeni zenizo. Ngakhale zikhale zokabvomerezera Mulungu yekha; kapena ndi zokabomerezera pamaso pa anthu ena amene asautsidwa nazo zoipa zathuzo; kapena ndi zodziwika kwa onse, ndipo ziyenera kubvomerezera pamaso pa anthu onse. Koma kubvomereza kuli konse kudzikhala koonadi kwa kuchula zoipa zeni zeni zimene iwe wacitazo.MOK 27.4

    M’masiku a Samueli, a Israyeli anapatukana ndi Mulungu. Iwo anali kusautsidwa cifukwa ca zoipa zawo; cifukwa anataya cikhulupiriro cao mwa Mulungu, nataya cizindikiro ca mphamvu zace ndi nzeru zace za kulamulira mtunduwo, nataya cikhulupiriro m’nzeru zace za kucinjiriza ndi kuonetsera nchito yace. Iwo adasiyana ndi wolamulira wa dziko lonse, nafuna kulamulidwa monga amitundu akuwazungulira. Asanapeze mtendere, anabvomereza momveka cotere: “Popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse, tinaonjeza coipa ici, ca kuti tinadzipemphera mfumu.” (1 Sam. 12: 19. ) Anabvomereza cimo leni leni limene anacitalo. Kusayamika kwawo kunasautsa miyoyo yao ndi kuwalekanitsa ndi Mulungu wawo.MOK 29.1

    Kubvomereza sikungalandiridwe kwa Mulungu ngati sikuli kulapa koona ndi kukonzanso. Koma m’moyo musinthike; cinthu ciri conse coipira Mulungu cicotsedwe. Izi zidzacitika ngati timva cisoni ndi zoipa zathu. Nchito imene tiyenera kucita pa mbali yathu idafotokozedwa bwino lomwe: “Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pa maso panga, lekani kucita zoipa; phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizam osautsidwa, weruzirani ana a masiye, munenere akazi a masiye.” (Yesaya 1: 16, 17. ) “Woipayo akabweza cikole, nakabweza ico anacilanda mwa cifwamba, nakayenda m’malemba a moyo, wosacita cosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.” (Ezek. 33: 15. ) Pa kunena za nchito ya kulapa Paulo ati: “Mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa, komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M’zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m’menemo.” (2 Akor. 7: 11. )MOK 29.2

    Pamene ucimo upha zitsimikizo za makhalidwe abwino, wocita zoipayo sazindikira zilema za makhalidwe ace, kapena kuzindikira kukula kwace kwa zoipa zimene iye wazicita; ndipo ngati sagonjera ku mphamvu yotsutsa ya Mzimu Woyera, adzangokhalabe mu mdima wosazindikira zoipa zace. Kubvomereza kwace sikuli koona mtima. Akapezedwa kuti wacita zoipa amangopeza mookanira, ndipo nthawi iri yonse akadzudzulidwa, amanena kuti kukadakhala kopanda cifukwa cakuti cakuti sindikadacita cimeneci.MOK 29.3

    Adamu ndi Hava atadya zipatso zokanizidwa zija anadzazidwa ndi manyazi ndi kuopsedwa. Poyamba anali kuganiza za kupeza mokanira coipa cawo, ndi kuti apulumuke ku ciweruzo coopsa ca imfa. Pamene Yehova anafunsa za cimo lao, Adamu anayankha, nakankhira coipaco mbali ina kwa Mulungu, mbali ina kwa mkazi wace: “Mkazi amene munandipatsa ine kuti akhale ndi ine, ameneyo anandipatsa ine za mtengo, ndipo ndinadya.” Mkazi anakankhira cimolo pa njoka nati, “Njoka inandinyenga ine, ndipo ndinadya.” (Gen. 3: 12, 13. ) Mudaipangiranji njoka? Mudailoleranji kudzalowa mu Edene? Zimenezi ndizo zifunso anafunsa popeza mokanira cifukwa ca zoipa zace, cotero anali kuda Mulungu cifukwa ca kulephera kwawo. Mzimu wa kudziyesera yekha wolungama unayambidwa ndi atate wa bodza, ndipo uli kuonekere mwa ana onse a Adamu. Kubvomereza kotere si kocokera mwa Mzimu wa Mulungu, ndipo sikudzalandiridwa ndi Mulungu. Kulapa koona kudzamtsogolera munthu kunyamula coipa cace yekha, ndi kucibvomereza wopanda cinyengo. Monga ngati wa msonkho uja, wosafuna ngakhale kuyang’ana maso ace kumwamba, adzapfuula, “Mulungu mundicitire cifundo ine wocimwa;” ndipo amene azindikira macimo awo adzayesedwa olungama, cifukwa Yesu adzapembedzera mwazi wace kuthangata moyo wolapa.MOK 30.1

    Zitsanzo za m’Mau a Mulungu za kulapa koona ndi kudzicepetsa zisonyeza mzimu wa kubvomereza kopanda kuzemba ucimo, kapena kudziyesera wolungama. Paulo sanafune kudzibisa yekha; iye afotokoza ucimo wace monga momwe uli, wosafuna kucepetsa coipa cace. Iye ati: “Ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m’ndende, popeza ndinalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo ndinabvomerezapo. Ndipo ndinawalanga kawiri kawiri m’masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene za mwano; ndipo pakupsa mtima kwakukuru pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira ku midzi ya kunja.” (Mac. 26: 10, 11. ) Sazengereza ponena kuti “Kristu anadza m’dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; mwa iwowa ine ndine woposa.” ( lTim. 1: 15. )MOK 30.2

    Mtima wosweka ndi wodzicepetsa, wogonjetsedwa ndi kulapa koona, udzazindikira za cikondi ca Mulungu ndi mtengo wace wa mtanda; ndipo monga mwana amabvomereza kwa atate wokonda, cotero wolapa woona ad2abwera nazo zoipa zace zonse pamaso pa Mulungu. Ndipo kudalembedwa, “Ngati tibvomereza macimo athu ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti akatikhululukire macimo athu ndi kutisambitsa kuticotsera cisalungamo ciri conse.” (1 Yohane 1: 9. )MOK 30.3

    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents