Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
  • Results
  • Related
  • Featured
No results found for: "".
  • Weighted Relevancy
  • Content Sequence
  • Relevancy
  • Earliest First
  • Latest First
    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents

    MUTU 3—KULAPA

    Kodi munthu adzakhala bwanji wolungama ndi Mulungu? Kodi wocimwa adzayesedwa bwanji wolungama? Tingathe kuyeretsedwa ndi kulumikizana ndi Mulungu mwa Kristu mokha; koma nanga tingadze bwanji kwa Kristu? Ambiri ali kufunsa cifunso comwe cinafunsidwa ndi makamu a anthu pa tsiku la Pentekoste, pamene anatsutsidwa za ucimo, iwo anapfuula, “Tidzacita ciani?” Mau oyamba a kuyankha kwa Petro anali akuti, “Lapani.” (Mac. 2: 38. ) Pa nthawi ina, pambuyo pace, iye anati, “Lapani,... ndipo bwererani kuti afafanizidwe macimo anu.” (Mac. 3: 19. )MOK 17.1

    Kulapa kutanthauza kucita cisoni ndi zoipa, ndi kuzisiya. Sitingausiye ucimo kufikira titaona kuipa kwace. Ngati sitingausiye kuyambira m’mitima moyo sungasinthike kweni kweni.MOK 17.2

    Alipo ambiri amene sazindikira makhalidwe a kulapa koona. Ambiri amacita cisoni kuti acimwa, ndipo amakonza kunja kwawo, cifukwa amaopa kuti zoipa zawo ziwatengera mabvuto. Koma uku si kulapa monga mwa nzeru ya Bible. Amalira cifukwa ca mabvutowo, osati cifukwa ca ucimo. Cisoni cotere ndi conga ca Esau pamene anaona kuti ukulu wace wamtaikira ku nthawi zonse. Balamu, poopsedwa ndi mngelo woima m’njira yace ndi lupanga losolola, anabvomereza zoipa zace kuti angataye moyo wace; koma sikunali kulapa cifukwa ca zoipa, sikunali kutembenukai, sananyansidwe ndi zoipa zace. Yudase Isikarioti, atapereka Mbuye wace, ananena, “Ndinacimwa pakupereka mwazi wosalakwa.” (Mateyu 27: 4. )MOK 17.3

    Anabvomereza cifukwa ca kuopa ciweruzo. Zimene zinali kudza kwa iye ndizo zinali kumuopsa, koma munalibe cisoni ceni ceni mu mtima mwace ca kuti wapereka Mwana wa Mulungu v/opanda cirema, nakana Woyerayo wa Israyeli. Farao, pamene anali kusautsidwa ndi maweruzo a Mulungu, anazindikira cimo lace, m’malo mwa kuti apulumuke cilangoco, koma anaumitsanso mtima miliriyo ikaletsedwa. Onsewa anali kulira cifukwa ca zobvuta zimene zinadza cifukwa ca ucimo, koma sanacite cisoni cifukwa ca zoipazo.MOK 17.4

    Koma pamene mtima ugonjera mphamvu ya Mzimu wa Mulungu, cikumbumtima cidzauka, ndipo wocimwayo adzazindikira kupatulika kwace kwa malamulo a Mulungu, maziko a ufumu wace m’mwamba ndi pa dziko lapansi.MOK 17.5

    “Kuunika kumene kuunikira munthu ali yense wakulowa m’dziko lapansi” (Yohane 1: 9), kumaunikira m’zipinda za mtseri za moyo, ndipo zobisika za mdima zimaonekera. Mtima umatsutsidwa. Wocimwayo amazindikira cilungamo ca Yehova, naopa kuonekera m’zoipa zace pamaso pa Wosanthula mitima. Iye aona cikondi ca Mulungu, kukoma ndi cimwemwe ca ungwiro; iye alakalaka kutsukidwa ndi kuyanjanitsidwa ndi Mulungu.MOK 19.1

    Pemphero la Davide atagwa, lisonyeza makhalidwe a cisoni coona ca zoipa. Kulapa kwace kunali koona ndi kocokera pansi pa mtima. Sanayese kubisa cimo lace; sanafune kupulumuka kuciweruziro; litero pemphero lace. Davide anaona kukula kwa zoipa zace; anaona kuipitsidwa kwa moyo wace; ananyansidwa nawo ucimo wace. Sanapempherere kukhululukidwa kokha, koma anapemphereranso mtima wangwiro. Iye analakalaka cimwemwe ca cilungamo, — kuti alumikizane ndi kuyanjana ndi Mulungu. Uku ndiko kunali kunena kwa moyo wace:MOK 19.2

    “Wodala munthuyo wokhululukidwa cimo lace; cokwiriridwa coipa cace. Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zace; ndimo mu mzimu mwace mulibe cinyengo.” (Salmo 32: 1, 2. ) “Mundicitire ine cifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize macimo anga. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundicotsera coipa canga. Cifukwa ndazindikira macimo anga; ndipo coipa canga ciri pamaso panga cikhalire.... Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbu woposa matalala. ... Mundilengere mtima woyera Mulungu, mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga. Musanditaye kundicotsa pamaso panu, musandicotsere Mzimu wanu woyera. Mundibwezere cimwemwe ca cipulumutso canu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize.... Mundilanditse ku mlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa cipulumutso canga; lilime langa lidzakweza nyimbo ya cilungamo canu.” (Salmo 51: 1-14. )MOK 19.3

    Kulapa kotere sikungathe kucitika ndi mphamvu yathu; kumacokera mwa Kristu mokha, amene anakwera kumwamba naninkha za ufulu kwa anthu.MOK 19.4

    Napa pamene amacimwirapo ambiri, cifukwa cace amalephera kulandira thandizo limene Kristu amafuna kuwapatsa. Iwo amaganiza kuti sangathe kudza kwa Kristu koma ngati ayamba kulapa, ndipo kuti kulapa ndiko kumakonza cikhululukiro ca macimo. Ndi zoonadi kuti munthu amayamba kulapa asanakhululukidwe; cifukwa ndi mtima wokha wosweka ndi wodzicepetsa umene umazindikira kuti usowa Mpulumutsi. Koma nanga wocimwayo kodi adziyamba kulindira kufikira atalapa asanadze kwa Yesu? Kodi kulapaku kukhale ngati copinga pakati pa wocimwa ndi Mpulumutsi?MOK 19.5

    Bible saphunzitsa kuti wocimwa koma ayambe walapa asanasamalire kuitana kwa Kristu, “Idzani kuno kwa Ine, nonsenu akulema ndi akutodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11: 28. ) Cimene cimatsogolera anthu kulapa ndi ubwino wocokera kwa Kristu. Petro anafotokoza zomveka kwa Israyeli, pamene anati, “Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lace la manja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israyeli kulapa, ndi cikhululukiro ca masimo.” (Mac. 5: 31. ) Sitingathe kulapa wopanda Mzimu wa Kristu kudzutsa cikumbumtima cathu, monga momwe sitingathe kulandira cikhululukiro wopanda Kristu.MOK 20.1

    Kristu ndiye kasupe wa zabwino zonse. Iye yekha ndiye angathe kuika udani wa ucimo mu mtima mwathu. Cilakolako ciri conse ca kucita zabwino ndi zoona, kutsutsidwa kuli konse kwa zoipa za m’mitima yathu, ndiwo umboni wakuti Mzimu wace uli kugwira nchito m’mitima yathu.MOK 20.2

    Yesu anati, “Ine, ngati nditukulidwa ku dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine ndekha.” (Yohane 12: 32. ) Kristu adzionetsedwa kwa wocimwa ngati Mpulumutsi amene anafera zoipa za dziko lonse; ndipo pamene tiona Mwana wa Nkhosa wa Mulungu pa mtanda, cinsinsi ca ciombolo ciyamba kuzindikirika m’mitima yathu, ndipo ubwino wa Mulungu utitsogolera ife kukulapa. Pa kufera ocimwa Kristu anaonetsa cikondi cosazindikirika: ndipo pamene wocimwa aona cikondi cimeneci, cimafewetsa mtima wace, ndipo moyo wace umamva cisoni ndi zoipa zace.MOK 20.3

    Zoonadi anthu ena nthawi zina amacita manyazi ndi njira zawo zoipa, nasiya makhalidwe awo ena oipa, asanazindikire kuti ali kukokedwa kunka kwa Kristu. Koma akafuna kukonzanso, ndi mtima wofuna kucita zabwino, ndi mphamvu ya Kristu imene iri kuwakokayo. Mphamvu imene iwo saidziwa imagwira nchito m’moyo, ndipo cikumbumtima cimauka ndipo moyo wa kunja umakonzedwanso. Ndipo pamene Kristu awakoka iwo kuyang’ana pa mtanda wace, kumuona Iye amene anapyozedwa ndi zoipa zawo, pompo malamulo amadza m’cikumbumtima mwawo. Kuipa kwa moyo wawo, zoipa za m’kati mwa moyo wawo zimaululidwa kwa iwo. Iwo amayamba kuzindikira za cilungamo ca Kristu, nanena, “Kodi ucimo nciani? poti udzifuna nsembe yotere pofuna kuombola amene adacimwa? Kodi cikondi conseci, kusautsidwa konseku, kucepetsedwa konseku, kunacitika kuti ife tisataike, koma tikhale nawo moyo wosatha?”MOK 20.4

    Wocimwayo atafuna nkukana cikondi cimeneci, ndi kukana kukokedwa kwa Kristu; koma ngati sangakane, adzakokedwa kudza kwa Yesu; kudziwa za nzeru ya cipulumutso kudzamtsogolera iye pa tsinde la mtanda pa kulapa zoipa zace zimene zinasautsa Mwana wokondedwa wa Mulungu.MOK 21.1

    Mtima umodzimodzi wa Mulungu umene uli kugwira nchito m’zinthu za cilengedwe uli kulankhula ndi mitima ya anthu, nuwalengera cilakolako ca kanthu kena kamene iwo alibe. Zinthu za dziko lapansi sizingathe kukwanitsa zolakalaka zawo. Mzimu wa Mulungu uli kuwapembedza iwo kuti afunefune zinthu zimene zingawapatse mtendere ndi mpumulo, — cisomo ca Kritsu ndi cimwemwe ca kuyera mitima. Ndi mphamvu zooneka ndi zosaoneka, Mpulumutsi wathu ali kugwira nchito nthawi zonse kukopa mitima ya anthu kuti asiye zokondweretsa zopanda pace za dziko lapansi, ndi kulandira madalitso osatha amene ali awo mwa Kristu. Kwa miyoyo yonseyi, imene iri kufunafuna kumwera m’mitsuko yosweka ya dziko lapansi, Uthenga wa Mulungu uti, “Iye wakumva ludzu adze. Ndi iye wofuna atenge madzi a moyo kwaulere.” (Cibvu. 22: 17. )MOK 21.2

    Inu amene m’mitima mulakalaka kanthu kabwino koposa kamene mungakapeze m’dziko lapansi muzindikira kuti cilakalako cimeneci ndi mau a Mulungu m’moyo mwanu. M’pempheni kuti akupatseni kulapa, kuti akuonetsereni Kristu m’cikondi cace cosatha ndi mu ungwiro wace wonse. M’moyo wa Mpulumutsi, maziko a cilamulo ca Mulungu—cikondi kwa Mulungu ndi kwa munthu zinasonyezedwa. Moyo wace unali wokonda, wopanda umbombo. Tidzaona kuipa kwa mitima yathu, pamene ife timuona Iye ndi kuwala kofumira kwa Mpulumutsi wathu.MOK 21.3

    Kapena tiri kungodzinyenga tokha monga anacita Nekodimo, kuti moyo uli wolungama, makhalidwe athu ali abwino, ndi kuganiza kuti sitifunika kudzicepetsa pamaso pa Mulungu monga wocimwa: koma pamene kuunika kwa Kristu kuwala m’ moyo mwathu, tidzaona zonyansa zathu: tidzazindikira umbombo wathu, ndi udani umene tiri nawo ndi Mulungu, zimene zimaipitsa nchito iri yonse ya moyo wathu. Pamenepo tidzadziwa kuti cilungamo cathu ciri nsanza zonyansa, koma mwazi wa Kristu wokha ndiwo ungatitsuke ife ku zoipa zonse nulenganso mitima yathu kukhala yofanana ndi Iye.MOK 21.4

    Ulemerero wa Mulungu pang’ono, ndi ungwiro wa Kristu pang’ono zitalowa m’moyo, konyansa kali konse ka mu mtima kadzaonekera bwino lomwe, nizionetsera poyera zifukwa ndi zofooka za makhalidwe a munthu. Zimaonetsera poyera zifuniro zoipa, kusakhulupirira kwa mtima, zonyansa za milomo. Makhalidwe osamvera a wocimwa amene amayesa cabe malamulo a Mulungu amaonekera poyera, ndipo mzimu wace umabvutidwa ndi mphamvu yakufunafuna ya Mzimu wa Mulungu. Amanyansidwa yekha pamene aona makhalidwe angwiro opanda banga a Kristu.MOK 21.5

    Pamene mneneri Danieli anaona ulemerero umene unazinga mthenga wa kumwamba amene anatumidwa kwa iye, anathedwa nzeru pa kuzindikira kufooka kwace ndi kusakonzeka kwace. Pa kufotokoza mphamvu ya cooneka cozizwitsaco, iye anati, “Koma wosakhala ndi mphamvu ine; pakuti kukomoka kwanga kunasandulika cibvundi, wosakhalanso ndi mphamvu ine.” (Danieli 10: 8. ) Moyo wokhudzidwa cotere udzadana ndi umbombo wace, ndi kudzikonda wokha, ndipo udzafunafuna, mwa cilungamo ca Kristu, mtima wangwiro umene uyanjana ndi malamulo a Mulungu ndi makhalidwe a Kristu.MOK 22.1

    Paulo ati kuti “Monga mwa cilungamo ca m’lamulo, “—monga mwa nchito za kunja kwa thupi, — iye anali “wosalakwa;” (Afilipi 3: 6) koma pamene anazindikira makhalidwe a uzimu a malamulo, anadziona yekha kuti ali wocimwa. Poweruzidwa ndi malamulo monga anthu anali kuonera ndi moyo wace wa kunja, iye anali wosacimwa; koma pamene anayang’anitsa m’kati mwa malamulo, nadziona yekha monga m’mene Mulungu anali kumuonera, iye anawerama m’kudzicepetsa nabvomereza zoipa zace. Iye ati, “Ndipo kale ine ndinali wa moyo popanda lamulo; koma pamene lamulo linadza, ucimo unatsitsimuka, ndipo ine ndinafa.” (Aroma 7: 9. ) Pamene iye anaona makhalidwe a uzimu a malamulo, ucimo unaonekera m’kuopsa kwace kweni kweni, ndipo kudzikweza kwace kunacoka.MOK 22.2

    Mulungu samaganiza kuti macimo onse ndi amodzimodzi kukula kwawo; iripo miyezo yosiyanasiyana ya ucimo, monga. m’mene ayesera anthu; koma ngakhale coipa cioneke cacing’ono m’maso mwa anthu, palibe chimo laling’ono pamaso pa Mulungu. Ciweruzo ca munthu ndi ca tsankho, ndiponso si cangwiro; koma Mulungu amayeza zinthu monga momwe ziri. Woledzera amanyozedwa, ndipo amauzidwa kuti ucimo wace udzamletsa kulowa kumwamba; pamene amaleka onyada, a umbombo ndi osirira osawadzudzula. Koma amenewa ndiwo macimo oipitsitsa pamaso pa Mulungu; cifukwa atsutsana ndi makhalidwe ace a cikondi, cikondi cimene cidzaza maiko onse osacimwa a kumwamba. Iye amene amagwa m’zoipa zazikuru, angamve manyazi ndi umphawi nadziwa kuti asowa cisomo ca Kristu; koma onyada saona kusowa, ndipo cotero amatsekera Kristu ndi madalitso osatha amene anadza kudzapereka.MOK 22.3

    Wa msonkho wosauka yemwe anapemphera, “Mulungu mundicitire cifundo ine wocimwa” (Luka 18: 13), anadziyesa yekha Wocimwa kwambiri, ndipo ena anali kumuyang’ana iye monga momwemo; koma iye anazindikira kusowa kwace, ndipo ndi katundu wa zoipa zace ndi manyazi anadza kwa Mulungu, napempha cifundo. Mtima wace unatsegukira Mzimu wa Mulungu kugvviramo nchito yace yacifundo ndi kummasula ku mphamvu ya ucimo. Pemphero ya Mfarisi lodzikuza ndi lodziyesera yekha wolungama linasonyeza kuti mtima wace unatsekeka kuti mphamvu ya Mzimu Woyera singathe kulowamo. Cifukwa ca kuti anali patari ndi Mulungu, sanazindikire kuipa kwace, pa kusiyana ndi makhalidwe opatulika a Mulungu. Analibe kusowa, ndipo cotero sanalandire kanthu.MOK 23.1

    Ngati uona kuipa kwako, usalindire kudzikometsa wekha. Alipo ambiri amene amaganiza kuti sali abwino kokwana kudza kwa Kristu. Kodi uli kuyembekeza kuti ukhala wabwino ndi kuyesa kwa iwe wekha? “Kodi Mkusi angathe kusintha khungu lace, kapena nyalugwe maanga ace? Pamenepo mungathe inunso kucita zabwino, inu amene muzolowera kucita zoipa.” (Yer. 13: 23. ) Cithangato cathu ciri mwa Mulungu mokha. Tisamalindira kukopa kolimba, nthawi yabwino, kapena makhalidwe oyera, koposa zimene tiri nazo. Sitingathe kucita kanthu mwa ife tokha. Tidzingodza kwa Kristu monga momwe tiri.MOK 23.2

    Koma ena asadzinyenge ndi kuganiza kuti, Mulungu, popeza ali wa cikondi ndi wa cisomo, adzapulumutsa ngakhale amene akana cisomo cace. Kuipa kwa ucimo kungathe kuyezedwa m’kuwala kwa mtanda. Pamene anthu amanena kuti Iye ali wabwino sangataye wocimwa, ayenera kuyang’ana pa mtanda. Kristu anasenza zoipa ndi kusamvera, nasautsidwa nafa m’malo mwa ocimwa, cifukwa ca kuti panalibe njira ina yopulumutsira munthu, cifukwa wopanda nsembe imenyi cinali cosatheka kupulumutsa anthu ku mphamvu ya zoipa, ndi kuyanjanitsidwa ndi oyera a kumwamba, — ndi kukhala olandirana nawo moyo wa uzimu. Cikondi, ndi masautso, ndi imfa ya Mwana wa Mulungu, zonsezi zicitira umboni kuopsa kwa ucimo, ndi kunena kuti, ngati moyo sudzipereka kwa Kristu, palibe kupulumuka ku mphamvu ya ucimo, palibe ciyembekezo ca moyo wa kumwamba.MOK 23.3

    Wocimwa nthawi zina amadzikhululukira okha pa kunena za amene adziyesera okha Akristu, “Ndine wabwino ngati iwo omwe. Sadzikana, sadziletsa, ndipo alibe makhalidwe koposa ine. Amakonda zokondweretsa ndi zofuna zawo monga ine ndemwe.” Motero amayesa zolakwa za ena mokanira kuleka nchito yawo. Koma zifukwa ndi zoipa za anthu ena sizikhululukira munthu ali yense; cifukwa Yehova sanatipatse ife citsanzo ca munthu wofooka wa ucimo. Mwana wa Mulungu wopanda banga ndiye citsanzo cathu, ndipo iwo amene amadandaula za njira yoipa ya amene adziyesera okha Akristu, iwowo ndiwo ayenera kusonyeza miyoyo yokoma ndi citsanzo cabwino. Ngati iwo amazindikira cimene Mkristu ayenera kucita, nanga cimo lawo siliri lalikuru? Iwo amadziwa cimene ciri cabwino, koma nakana kucicita.MOK 24.1

    Pewani kuzengereza. Musaleke nchito ya kusiya zoipa zanu, ndi kufuna mtima woyera mwa Kristu. Ambirimbiri amacimwira pamenepa, nataika kosatha. Sindinena kwambiri za kuti moyo uli waufupi ndi wosadziwika kukhala kwace; koma ciripo coopsa cacikuru — coopsa cosazindikirika — pa kucedwa kugonjera mau odandaula a Mzimu wa Mulungu, ndi kusankha kukhala m’zoipa; cifukwa kucedwako ndi kumeneku. Cimo, ngakhale licepe, adzataika nalo kosatha munthu wakuliumirirayo. Cimene siticigonjetsa, cidzatigonjetsa ife, ndipo cidzationongetsa.MOK 24.2

    Adamu ndi Hava anadzinyenga okha kuti m’kanthu kakang’ono kotere, kungodya zipatso zokanizidwa, sikungaoneke zoopsa zotere zonga zimene Mulungu adaneneratu. Koma kanthu kakang’onoka kunali kuswa malamulo opatulika a Mulungu, ndipo kanamlekanitsa munthu ndi Mulungu, ndi kutsegulira imfa ndi matsoka osaneneka m’dziko lathu. Mbadwo ndi mbadwo uli kulira pa dziko lapansi, ndipo cilengedwe conse ciri kubuula ndi kusautsika ndi zowawa cifukwa ca kusamvera kwa munthu. Kumwamba kudamvanso cimaliziro ca kupandukira Mulungu kwaceko. Mtanda umaima ngati cikumbutso ca nsembe yozizwitsa imene inacitika kupembedzera cifukwa ca kuswa malamulo a Mulungu. Tisauyang’ane ucimo ngati cinthu cacing’ono.MOK 24.3

    Kacimo kali konse, kukana cisomo ca Kristu, ziri kucita kanthu pa moyo wako; ziri kuumitsa mtima wako, ziri kucepetsa cifuniro, ziri kuumitsa mphamvu ya kuzindikira, ndipo ziri kucepetsa mphamvu yako ya kugonjera kudandaula kwa Mzimu Woyera wa Mulungu.MOK 24.4

    Ambiri ali kutonthoza cikumbumtima cobvutika pa kuganiza kuti adzasintha njira yoipayo nthawi ina akadzafuna; kuti adzingosewera ndi kuitana kwa cifundo, ndipo namangopembedze- dwabe kawiri kawiri. Iwo amaganiza kuti atanyoza Mzimu wa cisomo, atataya mphamvu yawo pa mbali ya Satana, pa nthawi yoopsa adzasintha njira yawo. Koma zimenezi sizimacitika mofewa. Macitidwe, maphunziro, a moyo wace, amanga makhalidwe kotero kuti nthawi imeneyi ndi owerengeka okha amafuna kulandira Uthenga wa Yesu.MOK 24.5

    Ngakhale koipa kamodzi, kacifuniro kamodzi koipa, kocitidwa dala, kadzacotsa mphamvu yonse ya Uthenga. Kacimo kali konse kamalimbitsa mtima kusakonda Mulungu. Munthu amene aonetsera kuuma mtima ndi kusakhulupirira coonadi, ali kungokolola zomwe iye yemwe adafesa. M’Bible monse mulibe kucenjeza kwina koopsa, konena kupewa kusewera ndi ucimo, koposa mau a munthu wa nzeru, kuti munthu wocimwa “adzamangidwa ndi zingwe za ucimo wace.” (Miyambo 5: 22. )MOK 25.1

    Kristu ali wofulumira kutimasula ku ucimo, koma iye sakakamiza cifuniro cathu, ndipo ngati cifuniro cathu ciumirirabe kucita zoipa, ndipo ife osafuna kumasulidwa, ngati ife sitifuna kulandira cisomo cace, nanga Iye angacitenji? Tadziononga tokha pakutsimikiza kukana cikondi cace. “Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso.” “Lero ngati mudzamva mau ace musaumitse mitima yanu.” (2 Akori. 6: 2; Heb. 3: 7, 8. )MOK 25.2

    “Pakuti munthu ayang’ana zooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mu mtima” (1 Sam. 16: 7), mtima wa munthu, ndi cimwemwe ndi cisoni cace, mtima woyendayenda wamphulupulu m’mene mukhalitsa zonyansa ndi cinyengo. Iye adziwa zotsimikiza zace zonse. Pita kwa iye ndi mtima wako woipitsidwa monga momwe uli. Monga Davide utsegulire kwa diso loona zonse, nunene, “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.” (Salmo 139: 23, 24. )MOK 25.3

    Ambiri amangolandira cipembedzo, maonekedwe ace okha, pamene mtima uli wosatsukidwa. Pemphero lanu likhale la kuti, “Mundilengere mtima woyera Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m’kati mwanga.” (Salmo 51: 10. ) Cita nawo moona moyo wako. Khala woona mtima, ndi wolimba mtima monga ngati uli kudziwa kuti moyo wako uli moopsa. Umenewu ndi mlandu woyenera kukonzedwa pakati pa moyo wako ndi Mulungu ku nthawi yosatha. Ngati uzengereza, osacita kanthu, udzaonongeka.MOK 25.4

    Phunzira mau a Mulungu ndi kupemphera. Mau amenewo adzakusonyeza m’malamulo a Mulungu ndi m’moyo wa Kristu maziko ace a kuyera mtima, wopanda zimenezo “palibe mmodzi adzaona Ambuye.” (Heb. 12: 14. ) Mauwo amatsutsa zoipa, amaonetsa njira ya cipulumutso. Asamalire, monga mau a Mulungu akulankhula ndi moyo wako.MOK 25.5

    Pamene muona kukula kwace kwa ucimo, pamene mudziona nokha monga momwe muli, musalephere. Kristu anadza kudzapulumutsa ocimwa. Ife sitifunika kumuuza Mulungu kuti ayanjane nafe, koma — Taonani cikondi cozizwitsa! —Mulungu mwa Kristu ali kuyanjanitsa dziko kwa Iye yekha.” 2 Akor. 5: 19. Iye ali kupembedza ndi cikondi cace mitima ya ana ace ocimwa. Palibe kholo lina pa dziko lapansi limene limapirira ndi zolakwa za ana ace, monga amacitira Mulungu ndi iwo amene afuna kuwapulumutsa. Palibe wina angathe kupembedzera wocimwa koposa Iye. Palibe milomo ya munthu imene imadandaulira munthu wosocera monga amacitira Iye. Malonjezano ace onse ndi macenjezo ace onse ali a cikondi cosaneneka.MOK 26.1

    Pamene Satana afika nakuuza kuti ndiwe wocimwa kwambiri, yang’ana kwa Mombolo wako, nulankhule za cifundo cace. Cimene cingakuthangate iwe ndiko kuyang’ana ku kuunika kwace. Zindikira zoipa zako, koma muuze mdaniyo kuti “Kristu anadza m’dziko lapansi kupulumutsa ocimwa” (1 Tim. 1: 15), ndi kuti iwe ungapulumutsidwe ndi cikondi cace cosatha. Yesu anafunsa Simoni za angongole awiri. Wina anamkongola mbuye wace ndalama pang’ono, koma wina anakongola ndalama zambiri; koma iye anawakhululukira onse awiriwo, ndipo Kristu anamfunsa Simoni,,, Ndi uti wa awa awiri anakonda mbuye wace koposa?” Simoni anayankha, “Iye amene anamkhululukira zoposa.” (Luka 7: 43. ) Ife tinacimwa kwambiri, koma Kristu anafa kuti ife tikhululukidwe. Nsembe yace iri yokwana kuonekera kwa Atate m’malo mwa ife. Iwo amene anawakhululukira zambiri adzamkonda koposa, ndipo adzaima pafupi ndi mpando wace kumtamanda Iye cifukwa ca cikondi cace cacikuru ndi nsembe yace yosatha. Timazindikira kuipa kwace kwa ucimo, pamene ife tizindikira kweni kweni cikondi ca Mulungu. Pamene ife tiona kutalika kwa unyolo umene unatsitsidwa cifukwa ca ife, pamene ife tizindikira za nsembe yosatha imene Kristu anaipereka cifukwa ca ife, mtima umasungunuka ndi kusweka ndi kudzicepetsa.MOK 26.2

    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents