Loading...
Larger font
Smaller font
Copy
Print
Contents
  • Results
  • Related
  • Featured
No results found for: "".
  • Weighted Relevancy
  • Content Sequence
  • Relevancy
  • Earliest First
  • Latest First
    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents

    MUTU 8—KUKULA KUFANANA NDI KRISTU

    Kusinthika kwa mtima kumene timasanduka nako ana a Mulungu, m’Bible kumalankhulidwa ngati kubadwanso. Ndiponso kumalankhulidwa ngati kumera kwa mbeu yabwino yodzalidwa ndi tsamunda. Monga momwemo iwo amene atembenukira kwa Kristu ali “monga makanda a lero,” kuti “akakule” (1 Petro 2: 2; Aefeso 4: 15) ku msinkhu wa amuna ndi akazi mwa Kristu Yesu. Kapena monga mbeu yabwino yofesedwa m’munda, iwo ayenera kukula ndi kubala zipatso. Yesaya ati kuti iwo “adzachedwa mitengo ya cilungamo, yakuioka Yehova, kuti alemekezedwe.” (Yesaya 61: 3. ) Cotero m’moyo wa cilengedwe, mumatengedwa mafanizo, kutithangata ife kumvetsetsa cinsinsi ca coonadi ca moyo wa uzimu.MOK 49.1

    Nzeru ndi luso la munthu sizingathe kupereka moyo ngakhale kwa kanthu kakang’ono mwa cilengedwe. Nyama kapena mtengo zingathe kukhala ndi moyo kupyolera mwa moyo umene Mulungu anaupereka. Cotero moyo wa uzimu umabadwa m’mitima ya anthu, kupyolera mwa moyo wocokera kwa Mulungu. Ngati munthu “sabadwa kucokera kumwamba” (Yohane 3: 3), sangathe kulandira moyo umene Kristu anadzaupereka.MOK 49.2

    Monga ndi moyo, coteronso ndi kukula. Ndi Mulungu amene amaturutsa mphundu nabalitsa maluwa zipatso. Mbeu imakula ndi mphamvu yace, “uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m’ngala’mo.” (Marko 4: 28. ) Ndipo mneneri Hoseya ati za a Israyeli kuti, “adzacita maluwa ngati kakombo.” “Adzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa.” (Hoseya 14: 5, 7. ) Ndipo Yesu atiuza “Lingalirani maluwa, makulidwe awo.” (Luka 12: 27. ) Mitengo ndi maluwa sizimakula ndi cisamaliro cawo, kapena kudera nkhawa kwawo, kapena ndi kuyesa kwawo, koma pa kulandira zimene Mulungu adazipereka za kutumikira moyo wawo. Mwana sangathe ndi nkhawa zace kapena mphamvu zace, kuonjezera msinkhu wace. Ngakhale inunso, ndi nkhawa zanu kapena kuyesa mwa inu nokha simungathe kukula mwa uzimu. Mtengo, mwana, zimakula pa kulandira zimene zimatumikira moyo wawo, — mpweya, dzuwa, ndi cakudya. Cimene zimacita mphatso za cilengedwezi kwa nyama ndi mitengo, ndizo amacita Kristu kwa iwo amene akhulupirira Iye. lye ndiye “Kuunika kwawo kosatha,” “dzuwa ndi cikopa.” (Yesaya 60: 19; Salmo 84: 11. ) Iye “adzakhala kwa Israyeli ngati mame.” “Iye adzatsika monga mvula pa maudzu.” (Hoseya 14: 5; Salmo 72: 6. ) Iye ndiye madzi a moyo. “Mkate wa Mulungu... wotsika kumwamba, ndi kupereka moyo ku dziko lapansi.” (Yohane 6: 33. )MOK 49.3

    Mu mphatso yaikuru ya Mwana wace, Mulungu anadzaza dziko lonse ndi cisomo cace, monga momwe mpweya umayenda kuzungulira dziko lonse. Onse amene asankha kupuma mpweya wopatsa moyowu adzakhala ndi moyo, nadzakula misinkhu yokwana amuna ndi akazi mwa Kristu Yesu.MOK 51.1

    Monga duwa limayang’ana ku dzuwa, kuti kuwala kwace kulithangate kulikometsa ndi kulifananitsa, coinco ifenso tidziyang’ana ku Dzuwa la Cilungamo kuti Kumwamba kuwale pa ife, kuti makhalidwe athu akule m’cifanizo ca Kristu.MOK 51.2

    Yesu aphunzitsa cinthu cimodzimodzici pamene ati, “Khalani mwa Ine, ndi Ine mwa Inu. Monga nthambi siingathe kubala cipatso pa yokha ngati siikhala mwa mpesa, motero mulibe inunso ngati simukhala mwa Ine... Wopanda Ine simungathe kucita kanthu.” (Yohane 15: 4, 5. ) Inu mumangilira pa Kristu kuti mukhale ndi moyo woyera, monga nthambi imangirira pa mtengo kuti ikule ndi kubala cipatso. Wopanda Iye mulibe moyo. Mulibe mphamvu ya kukana mayeso kapena kukula m’cisomo ndi m’kuyera mtima. Mukakhala mwa Iye, mudzakula. Mukamatunga moyo wanu kwa Iye, simudzafota kapena kukhala opanda zipatso. Mudzakhala ngati mtengo wookedwa m’mbali mwa madzi.MOK 51.3

    Ambiri amaganiza kuti ayenera kugwira mbali ina ya nchito okha. Anakhulupirira kuti Yesu awakhululukira zoipa zawo, koma tsopano ali kufuna kukhala bwino ndi kuyesa kwawo kokha. Koma kuyesa kuli konse kotere kuyenera kucotsedwa. Yesu ati, “Wopanda Ine simungathe kucita kanthu.” Kukula kwathu m’cisomo, cimwemwe cathu, kufunika kwathu, — zonse ziri pa kugwirizana ndi Kristu. Pa kulankhula ndi Iye, tsiku liri lonse, ora liri lonse, — pa kukhala mwa Iye, — tidzakula m’cisomo. Si woyamba yekha, komanso wotsiriza wa cikhulupiriro cathu. Kristu ndiye woyamba ndi wotsiriza ndi wa masiku onse. Iye adzakhala nafe, si kumayambiro kokha ndi kumapeto kwa ulendo wathu, koma pa phazi liri lonse la pa njira. Davide ati, “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse: popeza ali pa dzanja langa la manja, sindidzagwedezeka.” (Salmo 16: 8. )MOK 51.4

    Kodi muli kufunsa, “Kodi ine ndikhala bwanji mwa Kristu?”— Monga momwe udamlandirira poyamba. “Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa lye.” “Wolungama adzakhala ndi moyo ndi cikhulupiriro.” (Akolose 2: 6; Heb. 10: 38. ) Udadzipereka kwa Mulungu, kukhala wace wathunthu, kumtumikira ndi kumvera Iye, ndipo udamlandira Kristu kukhala Mpulumutsi wako. Sukadatha wekha kupembedzera zoipa zako kapena kusintha mtima wako; koma pa kudzipereka kwa Mulungu, udakhulupirira kuti Iye adakucitira zonsezi cifukwa ca Kristu. Ndi cikhulupiriro udasanduka wa Kristu, ndipo mwa Kristu udzakula mwa Iye, — pa kupereka ndi kulandira. Upereke zonse, — mtima wako, cifuniro cako, nchito yako, — kudzipereka kwa Iye kumvera zofuna zace zonse; ndipo utenge zonse, — Kristu, cidzalo ca madalitso onse, kukhala mu mtima mwako, kukhala mphamvu zako, cilungamo cako, mthangati wako wosatha, — kukupatsa mphamvu ya kumvera.MOK 51.5

    Udzidzipereka kwa Mulungu pa m’mawa; imeneyi ikhale nchito yako yoyamba. Pemphero lanu likhale lakuti, “Nditengeni Yehova, ndikhale wanu ndense. Ndiika zolinganiza zanga zonse pa mapazi anu. Mucite nane lero mu nchito yanu. Khalani ndi ine, nchito zanga zonse zicitike mwa Inu.” Zimenezi zidzicitika tsiku liri lonse. M’mawa uli wonse udzipereke kwa Mulungu kwa tsiku limenelo. Pereka zolinganiza zako zonse kwa lye, kuti uzicite kapena uzileke monga mwa kutsogolera kwace. Cotero tsiku ndi tsiku udzapereka moyo wako m’manja a Mulungu, motero moyo wako udzaumbidwa kufanana ndi moyo wa Kristu.MOK 52.1

    Moyo wa mwa Kristu ndi moyo wa mpumulo. Kapena simudzakhala cimwemwe cacikurukuru cakutooneka ndi kunja komwe, koma mudzakhala mtendere wacete wa cikhulupiriro. Ciyembekezo cako siciri mwa iwe wekha; koma mwa Kristu. Zofooka zako zalumikizana ndi mphamvu yace, kusadziwa kwako ndi nzeru zace, kulefuka kwako ndi mphamvu zace zosatha. Cotero usayang’ane kwa iwe wekha, usaganize za iwe wekha, koma yang’ana kwa Kristu. Uganize za cikondi cace, za ubwfno wace, za ungwiro wace, za makhalidwe ace. Moyo wathu udziganiza za Kristu m’kudzikana kwace, Kristu m’kudzicepetsa kwace, Kristu m’kuyera kwace, za Kristu m’cikondi cace cosayerekezeka. Udzasandulika m’cifaniziro cace pa kumkonda Iye, pa kumtsanza Iye, pa kutsamira pa Iye.MOK 52.2

    Yesu ati, “Khalani mwa Ine.” Mau amenewa amatipatsa ife mpumulo, kukhazikika, cikhulupiriro. Kawirinso aitana, “Idzani kuno kwa Ine... ndipo ndidzakupumulitsani inu.” (Mateyu 11: 28, 29. ) Mau a Davide atsimikiza ganizo lomweli: “Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye.” Ndipo Yesaya atsimikiza, “M’kukhala cete ndi m’kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu.” (Salmo 37: 7; Yesaya 30: 15. ) Mpumulo umenewu supezeka mu ulesi; cifukwa lonjezano la Mpulumutsi lakuitanira mpumulo lalumikizana ndi kuitana kwa nchito: “Senzani gori langa pa inu,... ndipo mudzapeza mpumulo.” (Mateyu 11: 29. ) Mtima umene upumuladi pa Kristu udzakhala wofunitsitsa ndi wa cangu kugwira nchito yace.MOK 52.3

    Pamene mtima uganizira za iwo wokha, umalekana ndi Kristu, kasupe wa mphamvu ndi moyo. Cifukwa cace nchito ya Satana masiku onse ndiyo kulekanitsa maganizo athu ndi Mpulumutsi, kuti moyo wathu ungalumikizane ndi kulankhulana ndi Kristu. Iye afuna kupatutsa mtima kuti uyang’ane zokondweretsa za dziko, zosamalira za moyo ndi zobvuta ndi cisoni, ndi zoipa za ena, kapena za iwe mwini. Usasoceretsedwe ndi macenjerero ace. Satana amatsogoleranso ambiri amene amazindikiradi, nafuna kukhala moyo wolungama kuganizitsa za zifukwa zawo ndi zofooka zawo, Iye amayembekeza kuwagonjetsa iwo pa kuwalekanitsa ndi Kristu. Ife tisamaganizitsa za ife eni koposa, ndi kuda nkhawa ndi kuopa ngati titi tidzapulumukedi. Zonse zoterezi zimalekanitsa moyo ndi Kasupe wa mphamvu zathu. Pereka kwa Mulungu moyo wako kuti akusungire, ndi kukhulupirira mwa Iye. Lankhula ndi kuganiza za Yesu. Kudzikonda wekha kutaike mwa Iye. Taya kukaika konse; cotsa mantha ako. Nena pamodzi ndi mtumwi Paulo, “Koma ndiri ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Kristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nawo tsopano m’thupi, ndiri nawo m’cikhulupiriro ca Mwana wa Mulungu, amene amandikonda nadzipereka yekha cifukwa ca ine.” (Agalatiya 2: 20. ) Pumula mwa Mulungu. Iye ali wakutha kusunga cimene iwe udamsungitsa. Ngati ungadzisiye wekha m’manja mwace, adzakupatsa mphamvu zoposa wogonjetsa mwa Iye amene anakukonda iwe.MOK 53.1

    Pamene Kristu anabvala makhalidwe a umunthu, Iye anadzimangirira yekha kwa anthu ndi mfundo ya cikondi imene singathe kuduka ndi mphamvu iri yonse koma ndi kusankha kwa munthu mwini wace. Masiku onse Satana amationetsera ife nyambo za kutikopa ife kuti tidule mfundo imeneyi, — kuti tisankhe kudzilekanitsa tokha ndi Kristu. Pamenepa ndipo tiyenera kuyang’anirapo, tilimbike, ndi kupemphera, kuti kena kasatikope ife kusankha mbuye wina; cifukwa nthawi zonse tiri omasuka kucita izi. Koma tiyeni timangirire maso athu pa Kristu, ndipo Iye adzatisunga ife. Pa kuyang’ana kwa Yesu tiri opulumuka. Pa- libe kena kangathe kuticotsa m’manja mwace. Pa kupenyerera kwa Iye kosalekeza, “tisandulika m’cithunzithunzi comweci kucokera ku ulemerero kunka ku ulemerero, monga ngati kucokera kwa Ambuye Mzimu.” (2 Akor. 3: 18. )MOK 53.2

    Ndimo m’mene akuphunzira oyamba anakhalira ofanana ndi Mpulumutsi wawo wokondedwa. Pamene ophunzirawo anamva mau a Yesu, iwo anamva mu mtima mwawo kuti amsowa Iye. Anamfuna, nampeza, namtsata Iye. Iwo anali naye m’nyumba, pa gome lodyera, m’cipinda, m’munda. Iwo anali naye monga asikolala ndi mphunzitsi wawo, masiku onse kulandira maphunziro a coonadi kucokera m’milomo yace. Iwo anamuyang’ana Iye, monga akapolo ayang’ana kwa mbuye wawo, kuphunzira nchito yawo. Akuphunzirawo anali anthu “akumva zomwezi tizimva ife.” (Yakobo 5: 17. ) Anali ndi nkhondo yomweyi ya zoipa. Anali kusowa cisomo comweci, pofuna kukhala ndi moyo woyera.MOK 54.1

    Ngakhale Yohane, wophunzira wokondedwayo, amene anaonetsera kvveni kweni cifaniziro ca Mpulumutsi, sanangobadwa nawo makhalidwe okondedwawa. Iye sanali wongokonda kuganiza za iye mwini kokha ndi wokonda ulemu, komanso anali wa nsontho ndi wokwiya msanga. Koma pamene makhalidwe a wa Kumwambayo anaonetsedwa kwa iye, anaona kuperewera kwace, ndipo anadzicepetsa yekha podziwa izi. Mphamvu ndi cipiriro, ulamuliro ndi cifundo, Ukulu ndi kufatsa zimene anaziona m’moyo wa masiku onse wa Mwana wa Mulungu, zinadzaza moyo wace ndi citamando ndi cikondi. Tsiku ndi tsiku mtima wace unakokedwa kunka kwa Kristu, kufikira analeka kuona za iye mwini cifukwa ca kukonda Mbuye wace. Makhalidwe ace okwiya ndi okonda ulemu anaperekedwa ku mphamvu yolenga ya Kristu. Mphamvu ya kulenganso ya Mzimu Woyera inalenganso mtima wace. Mphamvu ya cikondi ca Kristu inasintha makhalidwe ace. Cimeneci ndico cimaliziro coonadi ca kulumikizana ndi Yesu. Pamene Kristu akhala mu mtima, makhalidwe onse amasinthika. Mzimu wa Kristu, cikondi cace, zimafewetsa mtima, zimagonjetsa moyo, ndi kuutsa maganizo ndi zolakalaka zofuna Mulungu ndi kumwamba.MOK 54.2

    Pamene Kristu anakwera kumwamba, maganizo a maonekedwe ace anali cikhalirebe ndi akuphunzira ace. Anali maonekedwe a umunthu wace, wodzala ndi cikondi ndi kuunika. Yesu, Mpulumutsi, yemwe anali kuyenda nawo, nalankhula nawo, napemphera nawo, amene analankhula mau a ciyembekezo ndi cisangalatso ku mitima yawo, uthenga wa mtendere ukali m’mi- lomo yace, anatengedwa kunka kumwamba kucokera kwa iwo, ndipo mau ace aja anabweranso kwa iwo, pamene mtambo wa angelo unamlandira Iye, —‘Ndipo onani, Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse kufikira cimaliziro ca nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28: 20. ) Iye anakwera kumwamba m’makhalidwe a umunthu. Iwo anadziwa kuti Iye ali patsogolo pa mpando wacifumu wa Mulungu, ali cikhalirebe Bwenzi lawo ndi Mpulumutsi wawo; ndi kuti cifundo cace sicinasinthike; Iye anali kumvabe cifundo ndi zisautso za anthu. Iye anali kupereka patsogolo pa Mulungu ubwino wa mwazi wace wa mtengo wapatli, nasonyeza mapazi ndi manja ace olasidwa, kukumbutsa mtengo umene adapereka kuombola anthu ace. Iwo anadziwa kuti Iye anapita kumwamba kuwakonzera iwo malo, ndi kuti adzabweranso kuwalandira iwo kwa Iye yekha.MOK 54.3

    Pamene anakomana pamodzi, atakwera kale, iwo anali ofunitsitsa kupereka zofunsa zawo kwa Atate m’dzina la Yesu. Ndi mtima woonadi iwo anagwada m’pemphero, nabwereza mau a citsimikizo, “Ngati mudzapempha Atate kanthu adzakupatsani inu m’dzina langa.... Pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.” (Yohane 16: 23, 24. ) Iwo anakweza pamwamba dzanja la cikhulupiriro ndi kutsutsana kolimba, “Kristu ndiye amene adafera, inde makamaka ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja la manja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.” (Aroma 8: 34. ) Ndipo Pentekoste anawatengera iwo Mnkhoswe, amene Kristu anati Iyeyo “adzakhala ndi inu.” Ndiponso Iye anati, “Kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Mnkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu.” (Yohane 14: 17; 16: 7. ) Cifukwa cace mwa Mzimu, Kristu anali kukhala m’mitima ya ana ace masiku onse. Kugwirizana kwawo ndi Iye kunali kopambana tsopano koposa pamene anali pamodzi nawo mwini wace. Kuunika, ndi cikondi, ndi mphamvu ya Kristu wokhala m’kati mwawo, zinawala mwa iwo, kotero kuti anthu, poona, “anazizwa; ndipo anawazindikira kuti anakhala pamodzi ndi Yesu.” (Mac. 4: 13. )MOK 55.1

    Zonse zimene Kristu akacitira ophunzira ace oyamba aja, afuna kucitira ana ace lero; cifukwa m’pemphero lotsiriza lija, kagulu ka akuphunzira katamzungulira, Iye anati, “Koma sindipempherera iwo okha, koma iwo akukhulupirira Ine, cifukwa ca mau awo.” (Yohane 17: 20. )MOK 55.2

    Yesu anatipempherera ife, ndipo anapempha kuti ife tikhale amodzi mwa Iye, monga Iye ali mmodzi ndi Atate. Ha! Kugwi- rizanadi nanga! Mpulumutsi anati za Iye yekha, “Sakhoza Mwana kucita kanthu pa yekha,” “koma Atate wokhala mwa Ine acitA nchito zace.” Pompo, ngati Kristu ali kukhala m’mitima yathu, adzagwira nchito mwa ife “kufuna ndi kucita komwe monga mwa kukoma mtima kwace.” (Afilipi 2: 13. ) Tidzagwira nchito monga anagwirira Iye; tidzaonetsera mzimu womwe adauonetsa Iye. Ndipo potero, pa kumkonda Iye ndi kukhala mwa Iye, “Tidzakula m’zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu, ndiye Kristu.” (Aefeso 4: 15. )MOK 55.3

    Larger font
    Smaller font
    Copy
    Print
    Contents